Ezekieli 11:24-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu ku dziko la Akasidi, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandicokera, nakwera.

25. Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova.

Ezekieli 11