Ezekieli 11:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno;

3. ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama.

4. Cifukwa cace uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.

Ezekieli 11