1. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, ku thambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a cifaniziro ca mpando wacifumu pamwamba pao.
2. Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wobvala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makara a moto ocokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndiri cipenyere ine.
3. Tsono akerubi anaima ku dzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzara bwalo la m'kati.