7. Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.
8. Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.
9. Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; ciri conse cinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.
10. Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.