Ezara 9:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ici? pakuti tasiya malamulo anu,

11. amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale colowa canu ndilo dziko lodetsedwa mwa cidetso ca anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga yina kufikira nsonga inzace ndi ucisi wao.

12. Cifukwa cace tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthwawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu colowa ca ku nthawi yonse.

13. Ndipo zitatigwera zonsezi cifukwa ca nchito zathu zoipa ndi kuparamula kwathu kwakukuru; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga moticepsera mphulupulu zathu, ndi ku tipatsa cipulumutso cotere;

Ezara 9