36. Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.
37. Ana a lmneri, cikwi cimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.
38. Ana a Pasuru, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.
39. Ana a Harimu, cikwi cimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.