Ezara 2:26-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ana a Rama ndi Gaba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.

27. Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.

28. Anthu a ku Beteli ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu.

29. Ana a Nebo, makumi asanu mphambu awiri.

30. Ana a Magabisi, zana limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi.

31. Ana a Elamu wina, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

32. Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.

33. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza asanu.

34. Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.

35. Ana a Senai, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.

Ezara 2