Estere 9:30-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Natumiza iye akalata kwa Ayuda onse, ku maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahaswero, ndiwo mau a mtendere ndi coonadi;

31. kukhazikitsa masiku awa a Purimu m'nyengo zao, m'mene Moredekai Myuda ndi mkazi wamkuru Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kupfuula kwao.

32. Ndipo kunena kwace kwa Estere kunakhazikitsa mau awa a Purimu; ndipo kunalembedwa m'buku.

Estere 9