Estere 2:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahaswero, anakumbukila Vasiti, ndi cocita iye, ndi comlamulidwira.

2. Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;

3. ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wace, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'cinyumba ca ku Susani, m'nyumba ya akazi; awasunge Hege mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;

4. ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkuru m'malo mwa Vasiti. Ndipo cinthuci cinamkonda mfumu, nacita comweco.

Estere 2