Eksodo 8:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse acule pa dziko la Aigupto.

6. Ndipo Aroni anatambasula dzanja lace pa madzi a m'Aigupto; ndipo anakwera acule, nakuta dziko la Aigupto.

7. Ndipo alembi anacita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa acule pa dziko la Aigupto.

8. Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andicotsere ine ndi anthu anga aculewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.

9. Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke aculewo, acokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha?

Eksodo 8