Eksodo 40:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Nubveke Aroni cobvala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatwa andicitire Ine nchito ya nsembe.

14. Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati;

15. nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andicitire nchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.

16. Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anacita.

17. Ndipo kunali, mwezi woyamba wa caka caciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa kacisi.

18. Ndipo Mose anautsa kacisi, nakhazika makamwa ace, naimika matabwa ace, namangapo mitanda yace, nautsa mizati ndi nsanamira zace.

19. Ndipo anayalika hema pamwamba pa kacisi, naika cophimba ca cihema pamwamba pace; monga Yehova adamuuza Mose.

20. Ndipo anatenga mboniyo, naiika mlikasa, napisa mphiko palikasa, naika cotetezerapo pamwamba pa likasa;

21. nalowa nalo likasa m'kacisi, napacika nsaru yocinga, nacinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.

Eksodo 40