4. Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.
5. Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa ciombedwe comweci; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.
6. Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolidi, yoloca ngati malocedwe a cosindikizira, ndi maina a ana a lsrayeli.
7. Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso kwa ana a Israyeli; monga Yehova adamuuza Mose.
8. Ndipo anaomba capacifuwa, nchito ya mmisiri, monga maombedwe ace a efodi; ca golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
9. Cinakhala camowamphwa; anaciomba capacifuwa copindika; utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi, cinakhala copindika.