3. Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.
4. Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.
5. Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa ciombedwe comweci; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.
6. Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolidi, yoloca ngati malocedwe a cosindikizira, ndi maina a ana a lsrayeli.