19. Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.
20. Koma woyamba wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.
21. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira nchito, koma lacisanu ndi ciwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.
22. Ndipo uzicita madyerero a masabata, ndiwo madyerero a zipatso zoyamba za masika a tirigu, ndi madyerero a kututa pakutha pa caka.
23. Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, katatu caka cimodzi.