24. ndipo uike zonsezo m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ace amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
25. Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zicite pfungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.
26. Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.
27. Ndipo upatule nganga va nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; ziri za Aroni, ndi za ana ace amuna;
28. ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ace amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israyeli; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israyeli, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.