Eksodo 28:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Uloce miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa nchito ya woloca miyala, monga malembedwe a cosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi,

12. Ndipo ulike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso ca ana a Israyeli; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ace awiri, akhale cikumbutso pamaso pa Yehova.

13. Ndipo upange zoikamo za golidi;

14. ndi maunyolo awiri a golidi woona; uwapote ngati zingwe, nchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.

15. Upangenso capacifuwa ca ciweruzo, nchito ya mmisiri; uciombe mwa ciombedwe ca efodi; uciombe ndi golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

16. Cikhale campwamphwa, copindika, utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi.

Eksodo 28