7. Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.
8. Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.
9. Upangenso bwalo la cihema; pa mbali yace ya kumwela, kumwela, pakhale nsaru zocingira zakubwaloza nsaru ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wace wa pa mbali imodzi mikono zana;
10. ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zikhale zasiliva.
11. Momwemonso pa mbali ya kumpoto m'utali mwace pakhale nsaru zocingira za mikono zana limodzi m'utali mwace; ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsicizo ndi mitanda yace zikhale zasiliva.
12. Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsaru zocingira za mikono makumi asanu; nsici zace zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.
13. Ndipo m'kupingasa kwace kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.