Eksodo 26:28-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo.

29. Ndipo uzikuta matabwa ndi golidi, ndi kupanga mphete zao zagolidi zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golidi.

30. Ndipo uutse kacisi monga mwa makhalidwe ace amene anakusonyeza m'phiri.

31. Ndipo uziomba nsaru yocinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi nchito ya mmisiri;

32. ndipo uicinge pa mizati inai ya mitengo wasitimu, zokuta ndi golidi; zokowera zao zikhale zagolidi, ndi makamwa anai asiliva.

Eksodo 26