Eksodo 22:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona nave, alipetu kuti akhale mkazi wace.

17. Atate wace akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa colipa ca anamwali.

18. Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.

19. Ali yense agona ndi coweta aphedwe ndithu.

20. Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.

Eksodo 22