1. Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha, kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo; ndi nkhosa zinai pa nkhosayo,
2. Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe camwazi.
3. Litamturukira dzuwa, pali camwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wace.
4. Akacipeza cakubaco ciri m'dzanja lace camoyo, ngakhale ng'ombe, kapena buru, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.
5. Munthu akadyetsa coweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula coweta cace, ndipo citadya podyetsa pa mwini wace; alipe podyetsa pace poposa, ndi munda wa mphesa wace woposa.
6. Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.