Eksodo 21:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. pamenepo mbuye wace azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wace amboole khutu lace ndi lisungulu; ndipo iye azimgwirira nchito masiku onse.

7. Ndipo munthu akagulitsa mwana wace wamkazi akhale mdzakazi, iyeyo asaturuke monga amaturuka anyamata.

8. Akapanda kumkonda mbuye wace, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu acilendo, popeza wacita naye monyenga.

9. Koma ngati amtomera mwana wace wamwamuna, amcitire monga kuyenera ana akazi.

Eksodo 21