Eksodo 19:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazicita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akubvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.

10. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zobvala zao,

11. nakonzekeretu tsiku lacitatu; pakuti tsiku lacitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse.

Eksodo 19