10. Ndipo Yoswa anacita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleki; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa citunda.
11. Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lace Israyeli analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lace Amaleki analakika.
12. Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ace, wina mbali yina, wina mbali yina; ndi manja ace analimbika kufikira litalowa dzuwa.