34. Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko.
35. Ndipo ana a Israyeli anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.
36. Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.