Eksodo 14:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israyeli anatukula maso ao, taonani, Aaigupto alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israyeli anapfuulira kwa Yehova.

11. Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwaticotsera kuti tikafe m'cipululu cifukwa panahbe manda m'Aigupto? Nciani ici mwaticitira kuti mwatiturutsa m'Aigupto?

12. Si awa maowo tinalankhula nanu m'Aigupto ndi kuti, Tliekeni, kuti tigwirire nchito Aaigupto? pakuti kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m'cipululu ai.

13. Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, cirimikani, ndipo penyani cipulumutso ca Yehova, cimene adzakucitirani lero; pakuti Aaigupto mwawaona lerowa simudzawaonansokonse.

Eksodo 14