20. Musadye kanthu ka cotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopandacotupitsa.
21. Pamenepo Mose anaitana akuru onse a Israyeli, nanena nao, Pitani, dzitengereni ana a nkhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paskha.
22. Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuubviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asaturuke munthu pakhomo pa nyumba yace kufikira m'mawa.
23. Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aaigupto; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woonongaalowe m'nyumba zanu kukukanthani.
24. Ndipo muzisunga cinthu ici cikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.