Eksodo 12:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu cikumbutso, muzilisunga la madyerero a Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la madyerero, likhale lemba losatha.

15. Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzicotsa cotupitsa m'nyumba zanu; pakuti ali yense wakudya mkate wa cotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lacisanu ndi ciwiri, munthu amene adzasadzidwa kwa Israyeli.

16. Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasacitike nchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzicita.

17. Ndipo muzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinaturutsa makamu anu m'dziko la Aigupto; cifukwa cace muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.

Eksodo 12