14. Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Aigupto, ndipo linatera pakati pa malire onse a Aigupto, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.
15. Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala cabiriwiri ciri conse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Aigupto.
16. Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.
17. Ndipo tsopano, ndikhululukirenitu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andicotsere imfa yino yokha.
18. Ndipo anaturuka kwa Farao, napemba Yehova.
19. Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Aigupto.
20. Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke.