8. M'Horebe momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani.
9. Muja ndinakwera m'phiri kukalandira ma gome amiyala, ndiwo magome a cipangano cunene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi.
10. Ndipo Yehova anapereka kwa ine magome awiri amiyala, olembedwa ndi cala ca Mulungu; ndipo panalembedwa pamenepo monga mwa mau onse amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku lakusonkhana.
11. Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a cipangano,
12. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawaturutsa m'Aigupto wa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.
13. Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira;