11. Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a cipangano,
12. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawaturutsa m'Aigupto wa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.
13. Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira;
14. undileke, ndiwaononge, ndi kufafaniza dzina lao pansi pa thambo; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi waukuru woposa iwo.
15. Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a cipangano anali m'manja mwanga.
16. Ndipo ndinapenya, taonani, mudacimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.