12. Ndipo kudzakhala, cifukwa ca kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwacita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani cipangano ndi cifundo cimene analumbirira makolo anu;
13. ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukucurukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi ana a nkhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.
14. Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.
15. Ndipo Yehova adzakucotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.