24. ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wace, ndi ukuru wace, ndipo tidamva liu lace ali pakati pa mote; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.
25. Ndipo tsopano tiferenji? popeza mote waukuru uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa.
26. Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife, nakhala ndi moyo?
27. Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzicita.
28. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; cokoma cokha cokha adanenaci.
29. Ha! mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti ciwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!