6. Rubeni akhale ndi moyo, asafe,Koma amuna ace akhale owerengeka.
7. Za Yuda ndi izi; ndipo anati,Imvani, Yehova, mau a Yuda,Ndipo mumfikitse kwa anthu ace;Manja ace amfikire;Ndipo mukhale inu thandizo lace pa iwo akumuukira.
8. Ndipo za Levi anati,Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu,Amene mudamuyesa m'Masa,Amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;
9. Amene anati za atate wace ndi amai wace, Sindinamuone;Sanazindikira abale ace,Sanadziwa ana ace omwe;Popeza anasamalira mau anu, Nasunga cipangano canu.
10. Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu,Ndi Israyeli cilamulo canu;Adzaika cofukiza pamaso panu,Ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu.
11. Dalitsani, Yehova, mphamvu yace,Nimulandire nchito ya manja ace;Akantheni m'cuuno iwo akumuukira,Ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.