Deuteronomo 33:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Rubeni akhale ndi moyo, asafe,Koma amuna ace akhale owerengeka.

7. Za Yuda ndi izi; ndipo anati,Imvani, Yehova, mau a Yuda,Ndipo mumfikitse kwa anthu ace;Manja ace amfikire;Ndipo mukhale inu thandizo lace pa iwo akumuukira.

8. Ndipo za Levi anati,Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu,Amene mudamuyesa m'Masa,Amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;

9. Amene anati za atate wace ndi amai wace, Sindinamuone;Sanazindikira abale ace,Sanadziwa ana ace omwe;Popeza anasamalira mau anu, Nasunga cipangano canu.

10. Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu,Ndi Israyeli cilamulo canu;Adzaika cofukiza pamaso panu,Ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu.

Deuteronomo 33