Deuteronomo 33:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Woyamba kubadwa wa ng'ombe yace, ulemerero ndi wace;Nyanga zace ndizo nyanga zanjati;Adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi.Iwo ndiwo zikwi khumi za Efraimu,Iwo ndiwo zikwi za Manase.

18. Ndi za Zebuloni anati,Kondwera, Zebuloni, ndi kuturukakwako;Ndi Isakara, m'mahema mwako.

19. Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;Apo adzaphera nsembe za cilungamo;Popeza adzayamwa zocuruka za m'nyanja,Ndi cuma cobisika mumcenga.

20. Ndi za Gadi anati,Wodala iye amene akuza Gadi;Akhala ngati mkango waukazi,Namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.

21. Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;Ndipo anadza ndi mafumu a anthu,Anacita cilungamo ca Yehova,Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.

Deuteronomo 33