6. Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena cakumwa colimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
7. Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, anaturuka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;
8. ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale colowa cao ca Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la hafu la Manase.
9. Cifukwa cace sungani mau a cipangano ici ndi kuwacita, kuti mucite mwanzeru m'zonse muzicita.
10. Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mapfuko anu, akuru anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israyeli;