Deuteronomo 29:26-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. napita natumikira milungu yina, naigwadira, milungu imene sanaidziwa, imene sanawagawira;

27. cifukwa cace Mulungu anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m'buku ili.

28. Ndipo Yehova anawazula m'nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi m'ukali waukuru, nawaponya m'dziko lina, monga lero lino.

29. Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zobvumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti ticite mau onse a cilamulo ici.

Deuteronomo 29