23. Kunena za Aavi akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao.)
24. Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, M-amori, ndi dziko lace m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
25. Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kucititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa cifukwa ca iwe.
26. Ndipo ndinatuma amithenga ocokera ku cipululu ca Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,
27. Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,
28. Undigulitse cakudya ndi ndarama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndarama, kuti ndimwe; cokhaci ndipitire coyenda pansi;
29. monga anandicitira ana a Esau akukhala m'Seiri, ndi Amoabu akukhala m'Ari; kufikira nditaoloka Yordano kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.