Deuteronomo 11:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. koma dziko limene mumkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba;

12. ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo cikhalire, kuyambira caka mpaka kutsiriza caka.

13. Ndipo kudzakhala mukasamalira cisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,

14. ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yace, ya myundo ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.

15. Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.

16. Dzicenjerani nokha, angacete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu yina, ndi kuipembedza;

Deuteronomo 11