15. Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.
16. Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso.
17. Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye ya ambuye; Mulungu wamkuru, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira cokometsera mlandu.
18. Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa cakudya ndi cobvala.