Deuteronomo 1:8-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.

9. Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;

10. Yehova Mulungu wanu anakucurukitsani, ndipo taonani, lero mucuruka ngati nyenyezi za kumwamba.

Deuteronomo 1