34. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,
35. Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.
36. Koma Kalebi mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ace; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.
37. Yehova anakwiya ndi inenso cifukwa ca inu, ndi kuti, lwenso sudzalowamo.
38. Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israyeli.