8. Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takucimwirani.
9. Ambuye Mulungu wathu ndiye wacifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;
10. sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ace anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ace aneneri.
11. Inde Israyeli yense walakwira cilamulo canu, ndi kupambuka, kuti asamvere mau anu; cifukwa cace temberero lathiridwa pa ife, ndi Ilumbiro lolembedwa m'cilamulo ca Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamcimwira.
12. Ndipo anakwaniritsa mau ace adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera coipa cacikuru; pakuti pansi pa thambo lonse sipanacitika monga umo panacitikira Yerusalemu.
13. Monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose coipa ici conse catidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kucita mwanzeru m'coonadi canu.