8. Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoza kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwace.
9. Ndipo mfumu Belisazara anabvutika kwambiri, ndi nkhope yace inasandulika, ndi akuru ace anathedwa nzeru.
10. Cifukwa ca mau a mfumu ndi akuru ace mkazi wamkuru wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakubvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;
11. pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkuru wa alembi, openda, Akasidi, ndi alauli;