15. Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace; koma sanakhoza kufotokozera kumasulira kwa cinthuci.
16. Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace, udzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwo.
17. Pamenepo anayankha Danieli, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwace.
18. Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi cifumu;
19. ndipo cifukwa ca ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, a manenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pace; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.