4. Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m'nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m'cinyumba canga,
5. Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingilira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandibvuta ine.
6. Cifukwa cace ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babulo, kuti andidziwitse kumasulira kwace kwa lotoli.
7. Pamenepo anafika alembi, openda, Akasidi, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitsa kumasulira kwace.