17. Pamenepo Danieli anapita ku nyumba kwace, nadziwitsa anzace Hananiya, Misaeli, ndi Azariya, cinthuci;
18. kuti apemphe zacifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa cinsinsi ici; kuti Danieli ndi anzace asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babulo.
19. Pamenepo cinsinsico cinabvumbulutsidwa kwa Danieli m'masomphenya a usiku. Ndipo Danieli analemekeza Mulungu wa Kumwamba.
20. Danieli anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, a pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zace;