6. Mwa pfuko la Aseri zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Nafitali zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri:
7. Mwa pfuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Levi zikwi khumi ndiziwiri:Mwa pfuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri:
8. Mwa pfuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Benjamini anasindikizidwa cizindikilo zikwi khumi ndi ziwiri.
9. Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikuru, loti palibe munthu anakhozakuliwerenga, ocokera mwa mtundu uti wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atabvala zobvalazoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao;
10. ndipo apfuula ndi mau akuru, nanena, Cipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.
11. Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wacifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi ku mpando wacifumu, nalambifa Mulungu,