Cibvumbulutso 2:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba;Izi azinena iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lace lamanja, iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi:

2. Ndidziwa nchito zako, ndi cilemetso cako ndi cipiriro cako, ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzicha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

3. ndipo uli naco cipiriro, ndipo walola cifukwa ca dzina langa, wosalema.

4. Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya cikondi cako coyamba.

Cibvumbulutso 2