22. Ndipo mau a anthu oyimba zeze, ndi a oyimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo nunisiri ali yense wa macitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;
23. 1 ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti 2 ndi nyanga yako mitunduyonse inasokeretsedwa.
24. Ndipo 3 momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.